Katakwe-Sonia Adadziwa Bwanji?

Katakwe

SONIA ADADZIWA BWANJI?

Wolemba: Lawrence Kadzitche 

 

Katakwe adangoti ndapata. Sonia adali msungwana wokongola komanso wakhalidwe losakaikitsa. Nkhani yakhalidwe imachokera poti mtsikanayo adali mtsogoleri wakwaya ndi wojijirika pa zochitika za achinyamata pampingo pomwe ankapemphera.

 

Katakwe adagwa m’chikondi ndi Sonia ndipo sadachedwe kutulutsa mawu ake a kukhosi. Monga msungwana wamwambo Sonia adalimbalimba kaye ndipo pomaliza adati khosi khoba amvekere ‘ndalora’. Apo chibwenzi chidayamba.

 

Poyamba iwo ankangocheza. Akati akakumane, Sonia ankakana. “Ine sindipanga nawo zachisawawa,” iye ankatero. “Tidzayamba kukhala malo amodzi pokhapokha tikadzamanga banja.”

 

Katakwe adatidi apa wapeza mngelo. “Aise, ndapeza kabuthu kamngwiro,” iye adanyadira kwa mzake wapamtima Likisho. “Sikalola za shotikati.”

 

Likisho adaseka. “Bwanawe, ali dere n’kulinga utayenda naye…”

 

“Ndayenda naye kumene,” Katakwe adamudula Likisho. “Sizimbayambaya zanuzi zogwa n’chiswe.”

 

“Aise, usanyoze…”

 

“Nanga ndikunama?” Katakwe adalimbikira. “Moti Sithandwa si sikalapu? Sikavenja wachabechabe.”

 

Likisho adalibe yankho. Ubwenzi wa Katakwe ndi Sonia udapitirira. Kaya udali mwayi, kaya chidali chani, tsiku lina Sonia adavomera kuti akakumane pa loji inayake. Bizinesi yaikulu ya lojiyi idali kupereka malo okumanira amuna ndi akazi kuti azichita zachisembwere.

 

Atafika, Katakwe ndi Sonia adapita pa reception. Wolandira alendo adatenga kiyi wa rumu 10 n’kumupatsa Katakwe.

 

“Rumu imeneyo ayi, babe,” Sonia adatero. “Nthawi yamasana ano mumatentha kwambiri. Akupatse rumu 15.”

 

Katakwe adadzidzimuka. Adaluka nsidze zake, maganizo akuthamanga. Mumatentha? Sonia adadziwa bwanji?

 

 

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

8 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *