Ntchito Zachifundo

Katakwe

NTCHITO ZACHIFUNDO

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

A Topitopi adatulutsa kabotolo kaphanthi kuchokera m’thumba la jekete lawo. Adayang’ana pomwe adalekeza bibidayo kenaka n’kuthira kukhosi. Adaipitsa kukamwa ngati abwira tsabola kwinaku akutseka botolo la kachasulo n’kulibwezeranso m’thumba.

 

“Mphwanga, ndinakuitanitsa kuti ndidzakulangize,” adatero malume akewo. “Mkazi wako anafika kunyumbaku kudzandidandaulira kuti ndalama zonse ukungothera zibwenzi.”

 

“Malume, mwakhala mukufika pakhomo paja,” adayankha Katakwe. “Pali chomwe mudaona kuti chikusowa?”

 

“Ayi,” adayankha mwachilungamo a Topitopi.

 

“Ana ndimawalipirira sukulu, lendi ndimalipira, kudya timadya bwino, ndiye vuto lili pati?”

 

A Topitopi adayendetsa dzanja lawo mtsitsi lawo lamzindo. “Nkhani ndiyakuti panopa ndalama zikuvuta kwambiri. Makobiri omwe umaonongera zibwenzizo udakamapangira chitukuko.”

 

Katakwe adagwedeza mutu. “Malume, nokha mwanena kale kuti ndalama zikuvuta nde mukuganiza kuti ndingamaononge ndalama?”

 

“Nanga poti ndizomwe apongozi anabwera kudzadandaula?”

 

“Malume, zomwe ndimachita ine ndintchito zachifundo osati kuononga ndalama,” adatero Katakwe. “Pali azimayi omwe akukhala m’tauni muno, kudya komanso kutumiza ana awo kusukulu chifukwa cha ine…”

 

A Topitopi adakweza dzanja.

 

“Musandidule, tsibweni. Suzeni ali ndi ana atatu, sianga, koma ndimawalipirira sukulu. Lidia lendi ndimamulipirira ndine. Anna kuti adye ndekuti ndamutumizira ndalama,” adatero Katakwe. “Zimenezo sintchito za chifundo?”

 

“Sindikumvetsabe…”

 

“Enanso mwa azimuna awowo kuti aphunzire n’chifukwa cha ntchito zachifundo zomwe azibambo ena adachitira amayi awo,” Katakwe adaunikira “Amai asamadzikonde. Pali ana ambiri omwe sadakaphunzira popanda amuna ngati ife kudzipereka, akazi ambiri omwe adakamagona ndi njala olo kuthamagitsidwa palendi pachipanda amuna ngati ife. Kodi amuna tonse titati ndalama zathu zizingokhala zathu ndi akazi athu, azimayi ndi ana amenewa angawathandize ndani?”

 

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

8 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *