Matenda A Abusa

Katakwe

MATENDA A ABUSA

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Akulu ampingowo adasonkhana kuti agwirizane chochita malinga ndi matenda a mbusa wamkulu wampingowo.

 

“Akulu ampingo, monga tonse tikudziwa, abusa athu adwala kwambiri,” adatero Bauzeni. “Ndimomwe ndikuonera, ndipofunika tipite nawo kuchipatala cha kunja kwadziko lino.”

 

“Mukunenadi zoona. Matenda amenewa ngofunika ku South Africa olo India,” adavomereza Nsikwa. “Ofunika tiuze akhrisitu akufuna kwabwino asonkhe ndalama.”

 

Katakwe adaimika mkono. “Atsogoleri anzanga, dzina la mpingo uno ndichani?”

 

“Jesus Never Fails Ministry,” adatero Bauzeni.

 

“Pachichewa silimatanthauza kuti Yesu Salephera?”

 

Onse adavomereza.

 

“Ndiye mukati tiwatumize kunja mukutanthauza kuti Yesu walephera kuwachiza abusawa?”

 

Funsoli lidawadzidzimutsa onse. Yona ndi amene adayankha. “Sitikutero…”

 

“Mukuti chani?”

 

Funsoli lidawavuta kuyankha. “Akuluakulu, musayiwale kuti akhrisitu athu akadwala, abusawa kapena ifeyo atsogoleri timawakapempherera. Mumpingo muno mwakhala anthu akudwala kuposanso abusawa koma sindinamveko wina akuti tiwasonkhere ndalama tiwatumize kuchipatala…”

 

“Atsogoleri…”

 

“Musandidule. Nthawi zonse nkhani imangokhala yoti timupempherere ndipo ambuye amukhudza…”

 

“Pa James 5 kuyambira verse 14 amati ngati wina wa inu akudwala itanani…”

 

“Eeetu, nkhani ili pamenepo. Kaya ndi mbusa kaya ndi nkhosa yadwala onse tiziwapanga zofanana. Ngati n’kupemphera onse apemphereredwe. Osati mbusa ndiye timusonkhere apite kuchipatala, m’khirisitu nde timupempherere. Chimenecho n’chiphamanso.”

 

End

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

2 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *