Katakwe- KWA ANKHOSWE

Katakwe

KWA ANKHOSWE

Wolemba: Lawrence Kadzitche

 

Udali mmawa, dzuwa litangotuluka kumene. Mkazi wa Katakwe adafika limodzi ndi Katakwe kunyumba kwa ankhosweko. Mwana wamkazi adali wokwiya ngati nkhuku yofuna kulandidwa mazira ndipo ankamukoka mwamuna wakeyo muja mayi wokwiya amachitira akagwira mwana wofukira.

 

“N’chani, apongozi?” adafunsa mkazi wa a Topitopi akuthira shuga m’tiyi yemwe adali m’chikapu chachikulu chapulasitiki.

 

“Apongozi, galu uyu wandionjeza,” adayankha ali wefuwefu mkazi wa Katakwe.

 

“Ugwireni mtima, apongozi,” mayi Topitopi adamudekhetsa mtima.

 

“Ndikuti akapanda kufotokoza bwino basi aliyense kwawo n’kwawo,” adatsimikiza mkazi wa Katakwe. “Bandi igawana zida.”

 

“Apongozi, nkhani sakamba choncho,” adaunikira mayi Topitopi. “Fotokozani bwino kuti tione pomwe pakhota nyani mchira.”

 

Mkazi wa Katakwe adapuma mozama. “Chitsiru ichi dzulo chinatsanzika kuti chikukacheza ndi anzake kumowa. Ine monga mkazi wokula ndi mwambo ndinachivomera. Mukudziwa nthawi yomwe chafika?”

 

Mmalo moyankha, mkazi Topitopi adakokera pafupi mbale yomwe mudali mabanzi n’kuyamba kumwa tiyi uja akumwera mabanziwo.

 

“Nyani ameneyu wafika pakati pa usiku, ndikutitu midinayiti,” adakalipa mkazi wa Katakwe. “Munthu woti ali pabanja n’kumachita zotero? Pang’onong’ono adakapeza n’tanyamuka.”

 

Mkazi Topitopi adamwetulira kwinaku akutafuna mabanzi aja.

 

“Ndiye ndafika pano kuti ankhoswe ake atiweruze,” adatsendera mkazi wa Katakwe.

 

“Nkhani yamveka, vuto ndilakuti ankhoswe mukufunawo palibe.”

 

“Palibe? Apita kuti mmamawa ngati uno?”

 

“Nawonso chichokere chadzana kupita kumowa sadafike mpaka pano,” adatero mkazi wa a Topitopi kwinaku akumwa tiyi.

 

Mkazi Katakwe adangoti chala ga pakamwa.

 

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

10 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *