Katakwe A TOPITOPI AMUYALUTSA

Katakwe
A TOPITOPI AMUYALUTSA
Wolemba: Lawrence Kadzitche

Kwa nonse omwe mumagwira ntchito, mukadzangomva kuti kwabwera wachibale wochokera kumudzi kuntchitoko, dzasiyeni zomwe mukuchita ndikukakumana naye nthawi yomweyo. Kaya mwatanganidwa bwanji, musadzalole wachibale wochokera kumudzi kukudikilirani pa reception.

Kaya chifukwa chiyani koma anthu amenewa amakonda kunena zinthu zosafunika kunena pagulu. Katakwe adazindikira izi nkhwangwa ili mmutu.

Pakampanipo Katakwe adali General Manager, mkulu woyang’anira kampani yonseyo. Adali munthu wofatsa, waulemu wake ndi wodziwa kuyendetsa bwino ntchito.

Tsikulo a Topitopi adabwera koyamba kudzamuchezera. Poti iye adali wotanganidwa, adawauza malume akewo kuti amudikire pa reception kuti awaperekeze kunyumba.

Padatenga nthawi kuti amalize zomwe amachitazo. Atatsiriza, adatuluka mu ofesi mwake kuti akakumane ndi tsibweni akewo.

Iye anadabwa kupeza malumewo atazunguliridwa ndi ma mesenjala, makilinala, azilonda ndi ogwira ntchito ena a pakampanipo. Ogwira ntchitowo, atawona iye watulukira, adachoka mozemba.

“Bwanji malume, mumapangitsa msonkhano?” iye adafunsa moseka ali m’galimoto ndi malumewo.

A Topitopi adaseka. “Asi. Ndimangocheza nawo.”

“Kucheza nawo? Onse aja ndimawawona ngati anali ndi chidwi chachikulu; mumacheza nawo zotani?”

Tsibweniwo adasekanso. “Ndimawuza kuti zakutsogolo sizidziwikadi. Sindinkadziwa kuti iweyo mphwanga n’kudzakhala bwana wotere.”

Katakwe adaluma mlomo wammunsi. “Mukutanthauza chiyani?”

“Uli mwanatu udadwala m’mimba mwa m’pwelele moti tinkangoti umwalira. Ayi koma udapulumuka.”

Katakwe adawaponyera diso.

“Kenaka udayamba zokomoka; khunyu. Moti tinkangoti uzelezeka. Ayi lero siuyu ndiwe bwana.”

“Tsono, malume, mumawauza anthu zimenezo?”

A Topitopi adaseka. “Ndimangokamba moseka. Motitu samakhulupirira n’tawauza kuti naa pagwamula udalibe mzake. Wakumbukira tsiku udagwa mmbuna lija akukuthamangitsa mchimwene wa Namagetsi?”

Katakwe sadakhulupirire kuti amanena izi ndi a Topitopi. “Tsono, tsibweni, inuyo anthuwa mukuti azindiwona bwanji pazonse mwanenazi?”

“Ndimangotitu adziwe zoti Mulungu ngwamkulu,” adayankha a Topitopi. “Koma zoti ana aja kuti ubereka tidachita kupezera fisi sindinanene.”

Katakwe adangoti kukamwa yasa ngati chambo chouma.

END

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

4 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *