Mkazi Amumasula

KATAKWE

MKAZI AMUMASULA

Wolembe: Lawrence Kadzitche

Kaya chidali chipongwe kapena kusalifuna banja, Katakwe adawonjeza. Chichokere chake masiku atatu apitawo, uku kudali kufika kwake. Iye adafika ali dzandidzandi, mowa uli m’nsidze.

“Bambo a Tumbizani, munali kuti?” adafunsa mkazi wake.

“Kuchibwenzi.”

“Chiani?” Naguguda adafunsa.

“Ngati mwayamba kugontha mkutu mundiuze ndipite nanu kwa sing’anga,” adatero Katakwe. “Ndati ndinali kwa wokondeka wanga.”

Mkazi wa Katakwe sadakhulupirire mawuwa. Inde zochita za Katakwe pakhomopo zimaonetsa kuti samafuna banja. Iye ankafika ataledzera n’kumamutukwana pazifukwa zosamveka. Inde iye ankamva mbiri yoti Katakwe adali ndi chibwenzi chamseri. Koma sadaganize kuti zidzafika poti Katakwe anene poyera m’maso muli gwa.

Ulendo uno udali wachiwiri kuti banjalo ligwedeze. Koyamba kudali patangotha chaka atangomanga banjalo koma nsalu ya lekaleka osaoneka pakhomopo. Nthawiyo Katakwe adafuna kuthetsa banja ponena kuti mkazi wakeyo adali wosabereka.

Mwamwayi Naguguda adapezeka wodwala apo nkhani n’kuzizira. Pano vuto lija lidali litaphukiranso ngati mbatata.

“Bambo, kulankhula bwanji kumeneku?”

“Ndati ngati pakhomo pano sipawoneka mwana wina basi banja latha,” adatero Katakwe

“Mphatso ya mwana imachokera kwa Ambuye,” adatero Naguguda. “Tiyeni tidikire.”

“Ndiyetu ukadikirira kwanu,” adatero motsimikiza Katakwe. “Ndapeza kale mkazi amene adzandiberekera mbumba.”

“Bambo…”

Katakwe adalitsakamula pama. “Chete! Banja apa latha. Lamwalira. Umange katundu wako. Ine undisiyire mwana wanga yekhayu basi.”

Naguguda adamuyang’ana Katakwe mwamwano. “Mwana wake uti?”

“Tumbizaniyu. Imeneyi ndi mbeyu yanga.”

Naguguda adaseka. Monyodola. “Adakuuzani kuti ndi mwana wanu ndani?”

Katakwe adati dzidzidzi.

“Uyutu ndidatola ndi mwamuna wina pongofuna kupulumutsa banjali mthawi ija munkati ndine wosabereka,” adatero mwana wamkazi. “Ndiye poti mwati banja latha, ndati ndikuwuzeni mungamadziyese wobereka apo muli gocho. Ngati simukukhulupirira tikhoza kukayesetsa DNA!”

End

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

4 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *