Katakwe Uthenga pa foni
By Lawrence Kadzitche
Udali msonkhano wa atsogoleri ampingowo wokambirana zochitika za nyengo ya pasaka. Abusa adali pomwepo ndipo Katakwe, ngati mtsogoleri wa Church Council, ndi amene ankatsogolera msonkhanowo. Kuti munthu asankhidwe mkulu wampingo, sangosankhidwapo. Amayang’ana zambiri. Ngakhale uzimu umakhala patsogolo, china chofunika kwambiri chimakhala khalidwe labwino. Motero kuti Katakwe asankhidwe mkulu wampingo zimatanthauza kuti mpingo udali wokhutitsidwa kuti khalidwe ndi moyo wake wauzimu zidali mchimake. Mwatsoka zinthu sizidali motere. Khalidwe ndi uzimu wa Katakwe zonse zidali za chiphamaso. Iye adali mmbulu mchikopa chankhosa. Kuseri khalidwe lake lidali lina. Izitu zidadziwika pamsonkhano wa akulu ampingowo. Zokambirana zidali mkati pamene foni ya mmanja ya Katakwe idalira. Idali imodzi mwa nambala zija sizionetsa amene wayimba. Posafuna kusokoneza msonkhano, Katakwe sadafune kuti ayankhe. Koma abusa adati, “Yankhani, atsogoleri; umadzanyozera foni yofunika.” Katakwe adayankha. Koma mphuno salota, sadadziwe kuti foniyo idali pa hands free, paja pakuti anthu ena amatha kumamva nawo zomwe ukulankhula. “Ola babe, bo bo!” mawu a chikazi adamveka. Katakwe adadzidzimuka ngati akumva mawu a malemu. Kukamwa kudatseguka ndi kutsekeka ngati kwa nsomba yovuulidwa mmadzi koma mawu sadatuluke. “Nthawi yomweyi ndakusowa kale, shuga,” msungwanayo adapitirira. “Dzana lija udandipatsa ya bo moti panopa ndikungomvabe tseke tseke mthupi ngati uchi.” Katakwe sadadziwe chakuti achite. Adafuna kuti adule foniyo koma monga muja zimachitira munthu akabalalika adapezeka kuti mmalo modula akukweza voliyumu. Mwina Katakwe adakanamizira kuti idali wrong number, kuti msungwanayo adaimbira munthu wolakwika. Koma sizidatero. “Ndimakukonda Katakwe,” msungwanayo adatero momveka bwino ngati msomali womaliza kukhomera bokosi lamaliro. “Darling Katakwe, you are my honey, my sugar, my chocolate. I love you,” ndipo msungwanyo adamaliza ndi kisi yomveka bwino kuti, “Muaaa!” Maso a onse adagwa pa Katakwe, akudikirira kuti afotokozapo chiyani pankhaniyi. End