Vuto Lili Pati

Katakwe

Vuto lili pati?

Wolemba: Lawrence Kadzitche

Katakwe adatulukira pakhomopo ali wefuwefu. Adangofikira kuvula ovololo yake n’kudziponya pampando.

“Ndimayendatu mothamanga kuti ndifike nthawi yabwino kuopa mbava,” iye adatero kwa mkazi wake. “Tandipatse madzi akumwa ndiwolobze ku m’mero.”

Mkazi wakeyo adakhala ngati sadamve. Iye adapitiriza kuonera filimu ya Nigeria ngati m’nyumbamo simunalowe munthu.

“Nasitoko, ndikuti tandipatsirako madzi ludzu landipha,” adabwereza Katakwe.

Mkazi wakeyo sadachotse maso ake pakanemayo. “Akudulani manja?”

Katakwe adamuyang’ana mwana wa mkaziyo modabwa. “Kodi Nasitoko, zinthu zikukhala bwanji masiku ano?”

“Zinthu ziti?” adafunsa mosasamala mwana wamkazi maso ake atamatirira pakanema uja.

“Masiku ano n’kakutumani kanthu simukumvera,” adafotokoza Katakwe. “Chilichonse mukumakana.”

Nasitoko adamuyang’ana mwamuna wakeyo ndi diso lodzaza ndi mwano. “Bambo, ano ndi masiku ena. Masiku a jenda. Nafe azimayi tatseguka m’maso. Nthawi yotipondereza idatha.”

Katakwe adapuma mozama. “Akukuponderezani ndi ndani?”

“Inuyo azibambo. Monga apapa mumati ndikakutungireni madzi chonsecho manja muli nawo. Masiku ano kaya n’kuphitsa madzi osamba, mudziphitsa nokha. Nsima muziphikanso. Mbale kutsuka nawo. Ngakhale kukolopa kumene, mudzikolopa. Nafe azimayi tipumule.”

“Mukutero! Inetu m’mayesa jenda imatanthauza amuna ndi akazi azitengana mofanana. Kufanana kwake kopatsana ulemu pazomwe wina angathe ndipo wina sangathe. Monga inuyo mukhoza kuyamwitsa mwana, ine sindingathe.”

“Sizimenezo, dala. Zonse dzichitireni. Kapu ndi iyo ili patebuloyo. Manja muli nawo, vuto lili pati?”

Katakwe adafuna alankhulepo koma adasiya. Iye adali atatopa ndiye sadalinso m’mudi yoti n’kulongolola. Itakwana nthawi yogona, iwo aja adakalowa m’gombeza.

Chifukwa chotopa Katakwe adagona tulo tofa nato. Adamudzutsa adali mkazi wake.

“Eee…bambo, tadzukani.” Katakwe adadzuka. “Ndikumva mapazi panjapa.”

Nthawi yomweyo adangomva phwaa, chitseko kuthyoledwa ndi chimwala. “Bambo, kwabwera akuba, takaonani.”

“Mayi, kaoneni ndinu,” Katakwe adayankha. “Angakangondikhapako.”

“Kulankhula kwa mtundu wanji kumeneko?” adafunsa Nasitoko. “M’mayesa mwamuna ndinu m’nyumba muno?”

“Ndiye?” adafunsa Katakwe akukokera bulangete.

“Ndine mkazi. Akhoza kukandichita chipongwe.”

Katakwe adaseka. “Mayi, masiku ano kuli jenda. Mwamuna ndi mkazi ngofanana. Mwayiwala kale zomwe mumanena zija? Chibonga ndi icho chili pakonacho. Manja muli nawo, vuto lili pati?”

End.

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *