Katakwe-M’DZIRA CHIMUGWIRITSA

Katakwe
CHOTULUKA M’DZIRA CHIMUGWIRITSA
Wolemba: Lawrence Kadzitche
Nthawi zina anthufe tikamachita zinthu tiziganiza kuti kodi tsogolo lake lidzakhala lotani. N’chifukwa chake amvula zakale amati kupha n’kupha, umakumbuka poguza.

Katakwe ankakhala ku Area 18 m’nyumba zija zokhala ndi makomo awiri. Mnyamata yemwe ankakhala khomo linalo dzina lake lidali Sofiasi. Katakwe ndi Sofiasi ankagwirizana ngati mapasa ndipo ankatchulana kuti “neba” ngati dzina lowonetsa chinzake.

Ngakhale nthiti zawo zimene zinkagwirizananso kwambiri. Zidali zonyaditsa- abambo ali, bwanawe bwanawe, amayi- amwali amwali. Kusiyana kwa maanja awiriwa kudali kwakuti banja la Sofiasi lidalibe ana pomwe la Katakwe lidadalitsidwa ndi ana atatu.

Katakwe ndi mkazi wa Sofiasi ankakonda kuselewulana. Tsiku lina ali awiri, Katakwe adati, “Kodi neba, iweyo ndi mchimwene uja, ali ndi vuto ndi ndani?”

Mkazi wa Sofiasi adaseka. “Ukufunsiranji?”

Katakwe adamwetulira. “Basi ndikuona nsalu ya lekaleka ikukuvutani ndiye ndimafuna ndichitepo kanthu.”

Mwana wamkazi adasekanso. “Koma nawenso! Ungachitepo chiani? Vutotu lili ndi anzanu aja. Ine ndili bwinobwino.”

“Ndiyetu tandipanga hayala ndilongosole zinthu,” adatero Katakwe akumupsinyira namwaliyo diso.

Nkhaniyi tsikulo idatha ngati yocheza. Koma kenaka, mkazi wa Sofiasi adayamba kuyitulutsa iye ndi Katakwe akakhala awiri. “Ndikudikiratu,” iye ankakumbutsa.

Mwana wamkazi sadadziwe kuti apa adangokankhira pumbwa kuchipwete. M’kuseka, m’chizake, m’kuzolowerana, awiriwo adayamba chibwenzi chamseri. Mkazi wa Katakwe sadadziwepo kanthu. Naye Sofiasi palibe chomwe adanunkhiza.

Kudapezeka kuti mkazi wa Sofiasiyo wayima. Sofiasi posadziwapo kanthu adaganiza kuti adapangitsa kuti duwa limasule ndiye.

“Anzanu timalera kaye,” iye adanyadira kwa Katakwe. “Sizanuzi zongothethetsa ana chisawawa ngati nkhuku.”

Katakwe adangoti lota, gocho wachabechabe, tabafungatira mazira ankhanga ngati nkhuku mimba ili yopereka ine. Mwana wamphongo adabadwa. Sofiasi adatenga Katakwe ndi mkazi wake kuti akawonere limodzi mphatsoyo. Mwana wamwamuna adalowa m’chipatalamo akuyenda modzipopa ngati finye kuti tsopano adali atavula mnyozo woti adali mtheno.

Mwina zinthu zidakatha bwino. Koma atangolowa, namwino adanyamula mwana uja namupatsa Katakwe. “Bambo, mwanatu ndiye wangokutengani ndendende,” adanyadira zambayo. “Ukutu ndiye kudzibereka.”

Amati chati deru chaopsa mlenje. Katakwe adaona maso a Sofiasi akugwa pankhope yake kenaka pa mwana uja. Zopenyerazo pobwereranso pa Katakwe zidali zodzazidwa ndi mkwiyo. Adaonanso mkazi wake akumuyang’ana mwa mafunso. Mwana wamwamuna adadziwiratu kuti chotuluka m’dzira chamugwiritsa!
END

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

5 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *