Katakwe- Paulendo

Katakwe
PAULENDO
Lawrence Kadzitche

Padali padepoti yabasi ya Wenela. Poyamba, Katakwe adaganiza kuti woyendetsa minibasiyo adangovala ndomayo ngati mwa manyado chabe. Chidali chipewa choluka cha mtundu wofiyira, golide ndi wobiriwira-mtundu uja anthu amati true colour or mbendera ya ma rasta. Adali mu T-Shirt yomwe pamtima padajambulidwa Peter Tosh ndikulembedwa mawu oti ‘Legalise It.” Nyimbo zomwe ankayika zidali za Reggae zokhazokha zamagulu ngati Culture, Burning Spear, Toots ndi ena otero.

Nthawi yomwe ankakwera basiyo, dilayivalayo adali bwino bwino. Katakwe adakhala pampando wakutsogolo n’kumacheza ndi shoveliyo akumvera nyimbo zija kwinaku anthu akumakwera minibasiyo.

Minibasiyo itatsala pang’ono kudzadza, dilaivalayo adatulutsa mfani wa chamba. “Man, ndikubwera ndikashambulire kaye tisanabanduke,” adatero Rastayo akupota ndudu.

“Kushambulira?” adafunsa Katakwe.

“Kukamenya kaya ka holy weed kuti makinawa tiwamenye bo,”

“Ukukasuta ukudziwa kuti uyendetsa basi?” Katakwe adafunsa modabwa.

“Man, ndikabanda nde ndimayendetsa bo,” dilayivalayo adafotokoza akutsika. “Chimenechi ndichakudya chathu ma Rasta chomwe tidachipeza chikumera chokha pamanda a mfumu Solomo.”

Kumene adapitako sadatenge nthawi. Koma mmene amafika adali atasinthiratu. Maso adali psu ngati anali m’khitchini.

“Man, mangani seat belt tikufuna tiyendetse mashini pasipidi ya ndege yamfiti,” dilayivalayo adalengeza akunyambita milomo yake yomwe tsopano idali gwa ngati amatafuna chinangwa chosaphika.

Dilayivalayo sadaname. Minibasiyo idachoka padepotipo ngati ikuthamangitsidwa ndi apolisi. Anthu onse m’basimo adangoti khuma ndi mantha kaamba ka liwiro la minibasiyo.

“Man, bwanji muchepetseko kasipidi,” Katakwe adapempha monyengerera. “Izitu ndizija sizidamuthere bwino Fadah.”

“Take it easy man,” Rastayo adatero akuonjezera moto. “Jah Rastafari will protect I and I.”

Katakwe adayang’ana kumbuyo kuti mwina anthu omwe anali mminibasimo amuthandiza. Koma ngakhale onse amaonetsa kuti sipidi ya dilayivalayo imawaopsa palibe adalankhula.

Atafika pa Ntcheu, dilayivala uja adatsika nkukasutanso kanundu woonjezera. “Refill, man. More fire! Selassie I!”

Adanyamukanso ndi liwiro loopsa. Katakwe adayang’anaso kumbuyo kuti mwina wina alankhulapo. Aliyense adangoti zi akuoneka wodandaula.

Ulendo udapitirira, Katakwe mumtima akuti akakafika ku Lilongwe ndi chisomo. Ngoziyo idachitikira mu Dedza pomwe dilaivalayo adalephera kukhota pakona ina yake yamsewu. Minibasiyo idasempha msewu, n’kusadabuzika katatu.

Mmene Katakwe amatsitsimuka adali m’chipatala. “Nokha mukuti dilaivala amasuta chamba komanso amayendetsa mosasamala, bwanji simunatsike?” adafunsa mkazi wake. “Anthu timatha kuona kuti dilaivala sakuyendetsa bwino koma osalankhulapo. Mathero ake zimakhala ngozi ngati izi.”

“Tikadamulamulira bwanji basi ili yake?” Katakwe adadziteteza.

“Nonse mudakatsika adakapitirira ulendo? Adakakumverani.”

Posowa choyankha, Katakwe adangoyamba kubuwula.

End

About the author

Lawrence Kadzitche

View all posts

9 Comments

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *