Katakwe
MATENDA A ABUSA
Wolemba: Lawrence Kadzitche
Akulu ampingowo adasonkhana kuti agwirizane chochita malinga ndi matenda a mbusa wamkulu wampingowo.
“Akulu ampingo, monga tonse tikudziwa, abusa athu adwala kwambiri,” adatero Bauzeni. “Ndimomwe ndikuonera, ndipofunika tipite nawo kuchipatala cha kunja kwadziko lino.”
“Mukunenadi zoona. Matenda amenewa ngofunika ku South Africa olo India,” adavomereza Nsikwa. “Ofunika tiuze akhrisitu akufuna kwabwino asonkhe ndalama.”
Katakwe adaimika mkono. “Atsogoleri anzanga, dzina la mpingo uno ndichani?”
“Jesus Never Fails Ministry,” adatero Bauzeni.
“Pachichewa silimatanthauza kuti Yesu Salephera?”
Onse adavomereza.
“Ndiye mukati tiwatumize kunja mukutanthauza kuti Yesu walephera kuwachiza abusawa?”
Funsoli lidawadzidzimutsa onse. Yona ndi amene adayankha. “Sitikutero…”
“Mukuti chani?”
Funsoli lidawavuta kuyankha. “Akuluakulu, musayiwale kuti akhrisitu athu akadwala, abusawa kapena ifeyo atsogoleri timawakapempherera. Mumpingo muno mwakhala anthu akudwala kuposanso abusawa koma sindinamveko wina akuti tiwasonkhere ndalama tiwatumize kuchipatala…”
“Atsogoleri…”
“Musandidule. Nthawi zonse nkhani imangokhala yoti timupempherere ndipo ambuye amukhudza…”
“Pa James 5 kuyambira verse 14 amati ngati wina wa inu akudwala itanani…”
“Eeetu, nkhani ili pamenepo. Kaya ndi mbusa kaya ndi nkhosa yadwala onse tiziwapanga zofanana. Ngati n’kupemphera onse apemphereredwe. Osati mbusa ndiye timusonkhere apite kuchipatala, m’khirisitu nde timupempherere. Chimenecho n’chiphamanso.”
End
Katakwe had a point.
It’s a tendency of akhristu ambiri amakonda kutekemeza azibusa as if azibusawu ndi Milungu. It’s high time now kumadzudzula mchitidwe umenewu. Alipo atumiki ambiri who are practicing this kusetekeka mmbusa at the expense of poor Christians.KULAKWITSA ZEDI.
Well said